Ezekiel 7

Chimaliziro Chafika

1Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:

“Chimaliziro! Chimaliziro chafika
ku ngodya zinayi za dziko.
3Chimaliziro chili pa iwe tsopano.
Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.
Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
4Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa
komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.
Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

5“Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:

“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!
Taona chikubwera!
6Chimaliziro chafika!
Chimaliziro chafika!
Chiwonongeko chakugwera.
Taona chafika!
7Inu anthu okhala mʼdziko,
chiwonongeko chakugwerani.
Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
8Ine ndili pafupi kukukwiyirani,
ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;
Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
9Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako
ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’

10“Taona, tsikulo!
Taona, lafika!
Chiwonongeko chako chabwera.
Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.
Kudzitama kwaphuka.
11Chiwawa chasanduka ndodo
yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.
Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.
Palibiretu ndipo sipadzapezeka
munthu wowalira maliro.
12Nthawi yafika!
Tsiku layandikira!
Munthu wogula asakondwere
ndipo wogulitsa asamve chisoni,
popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
13Wogulitsa sadzazipezanso zinthu
zimene anagulitsa kwa wina
chinkana onse awiri akanali ndi moyo,
pakuti chilango chidzagwera onsewo
ndipo sichingasinthike.
Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense
amene adzapulumutsa moyo wake.

14“Lipenga lalira,
ndipo zonse zakonzeka.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,
pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
15Ku bwalo kuli kumenyana
ndipo mʼkati muli mliri ndi njala.
Anthu okhala ku midzi
adzafa ndi nkhondo.
Iwo okhala ku mizinda
adzafa ndi mliri ndi njala.
16Onse amene adzapulumuka
ndi kumakakhala ku mapiri,
azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.
Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
17Dzanja lililonse lidzalefuka,
ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
18Iwo adzavala ziguduli
ndipo adzagwidwa ndi mantha.
Adzakhala ndi nkhope zamanyazi
ndipo mitu yawo adzameta mpala.

19“Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu
ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.
Siliva ndi golide wawo
sizidzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,
kapena kukhala okhuta,
pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
20Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka
ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.
Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa
kukhala zowanyansa.
21Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.
Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda
ndi kudziyipitsa.
22Ine ndidzawalekerera anthuwo
ndipo adzayipitsa malo anga apamtima.
Adzalowamo ngati mbala
ndi kuyipitsamo.

23“Konzani maunyolo,

chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo
ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
24Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa
kuti idzalande nyumba zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu
pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
25Nkhawa ikadzawafikira
adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
26Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,
ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.
Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.
Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,
ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
27Mfumu idzalira,
kalonga adzagwidwa ndi mantha.
Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.
Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,
ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Copyright information for NyaCCL